MBIRI YA MOYO WA TIMOTHY MTAMBO
Timothy Pagonachi Simbega Mtambo anabadwa pa 12 August m’chaka cha 1984 ku Chitipa. Iye ndi wachinayi kubadwa m’banja la ana 8 ndipo amachokera m’mudzi wotchedwa Simbega komwe iye mwini ndi mfumu.
Chizindikiro cha ufumu ndi zibangiri ziwiri zoyera zomwe amavala m’mikono mwake. Zibangiri ziwirizi ndi za zaka zoposa 200 ndipo munthu amapatsidwa akavekedwa ufumu.
Timothy anayamba sukulu ya pulayimale ali ku Zambia m’nthawi yomwe bambo ake ankagwira ntchito kumigodi m’dzikolo. Atabwelera kuno kumudzi, Timothy anapitiliza maphunziro ake pa Isharikira Primary School.
Atalemba mayeso ake a sitandade 8, iye anasankhidwa kukachita maphunziro asekondale pa Yamba CDSS koma mayeso a MSCE analembera pa Twanda Private School.
Kenako, anachita mwayi ndi kusankhidwa kukachita maphunziro aukachenhede otchedwa Bachelors of Arts (Humanities) ku University of Malawi mumzinda wa Zomba, sukulu yomwe iye ankaikhumbira zedi kuyambira ali wachichepere. Iye amati ankafunitsitsa kupita kusukuluyi chifukwa ankachita chidwi ndi nkhani yomenyera ufulu ndi chilungamo. Anthu omwe ankamuchititsa chidwi ndi MacDonald Sembereka, Moses Mkandawire ndi Undule Mwakasungula.
Ali kusukulu yaukachenjede, iye anakhalapo woyankhulira gulu lomwe limaimilira ana asukulu (Speaker of Students Union of Chancellor College).
Kuonjezera pamaphunziro atchulidwawa, Timothy ali ndi Master of International Cooperation and Development yomwe anaipeza m’chaka cha 2017 kuchokera ku University of Pavia-International mumzinda wa Lombardia ku Italy.
Timothy yemwe ndi nduna yakale yophunzitsa anthu ndi mgwirizano wa mdziko anagwiraponso ntchito ngati child protection worker ku Chitipa District Council, child protection worker ku Ministry of Gender komanso ngati wapampando wa bungwe la HRDC.
M’chaka cha 2020, Timothy anatula pansi udindo kubungwe la HRDC ndi kuyambitsa gulu la Citizens for Transformation (CIT) lomwe linathandizira nawo kukopa anthu kuti avotere Tonse Alliance m’chaka chomwecho.
Chinthu china chochititsa chidwi n’chakuti Timothy amayankhula ziyankhulo zopitilira khumi. Zina mwaziyankhulozi ndi Ndari, Mambwe, Ngonde, Sukwa, Tumbuka, Nyakusa ndi Lambya.
Iye amati zimamukhudza anthu ena akamafalitsa kuti iye si wakuno, pazifukwa zandale.
Timothy ali pabanja. Iye anakwatira Shally Natasha Mtambo yemwe ndi lawyer. Awiriwa ali ndi ana atatu omwe ndi Peace, Freedom ndi Justice.
Shally ali ndi Master in Energy Law kuchokera ku Vermont Law School m’dziko la United States of America.